Add parallel Print Page Options

Mawu a Bilidadi

18 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

“Kodi iwe Yobu utsiriza liti zoyankhula zakozi?
    Khala munthu wozindikira zinthu ndipo ukatero ife tidzayankhula.
Chifukwa chiyani ukutiyesa ngati ngʼombe
    ndi kuoneka ngati opusa mʼmaso mwako?
Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako,
    kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo?
    Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake?

“Nyale ya munthu woyipa yazimitsidwa;
    malawi a moto wake sakuwalanso.
Kuwala kwa mʼnyumba mwake kwasanduka mdima;
    nyale ya pambali pake yazima.
Mayendedwe ake amgugu azilala;
    fundo zake zomwe zamugwetsa.
Mapazi ake amulowetsa mu ukonde
    ndipo akungoyendayenda mu ukondewo.
Msampha wamkola mwendo;
    khwekhwe lamugwiritsitsa.
10 Amutchera msampha pansi mobisika;
    atchera diwa pa njira yake.
11 Zoopsa zikumuchititsa mantha kumbali zonse,
    zikutsatira mayendedwe ake onse.
12 Mphamvu zake zatha chifukwa cha njala,
    tsoka likumudikira.
13 Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse;
    miyendo yake, manja ake, zonse zawola.
14 Wachotsedwa mʼnyumba imene ankadalira,
    ndipo amukokera ku imfa, mfumu ya zoopsa zonse.
15 Mʼnyumba mwake zonse zachotsedwamo;
    awazamo sulufule kuti aphe tizirombo ta matenda.
16 Mizu yake ikuwuma pansi
    ndipo nthambi zake zikufota
17 Sadzakumbukiridwanso pa dziko lapansi;
    sadzakhalanso ndi chinthu chomutchukitsa mʼdziko.
18 Amuchotsa pa malo owala ndi kumuponya ku mdima,
    ndipo amupirikitsa pa dziko lonse.
19 Iye alibe ana kapena zidzukulu pakati pa anthu ake,
    kulibe wotsala kumene iye ankakhala.
20 Anthu akumadzulo adabwa kwambiri ndi tsoka lake;
    anthu akummawa agwidwa ndi mantha aakulu.
21 Ndithudi, izi ndiye zimagwera munthu woyipa;
    amenewa ndiye mathero a munthu amene sadziwa Mulungu.”