Add parallel Print Page Options

Mawu a Yobu

16 Pamenepo Yobu anayankha kuti,

“Ndinamvapo zambiri monga zimenezi;
    nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu.
Kodi mawu anu ochulukawo adzatha?
    Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?
Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu,
    inuyo mukanakhala monga ndilili inemu;
Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu
    ndi kukupukusirani mutu wanga.
Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani;
    chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu.

“Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa;
    ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe.
Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu;
    mwawononga banja langa lonse.
Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni;
    kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa.
Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane,
    amachita kulumira mano;
    mdani wanga amandituzulira maso.
10 Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza;
    amandimenya pa tsaya mwachipongwe
    ndipo amagwirizana polimbana nane.
11 Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa
    ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima.
12 Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya;
    anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya.
Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;
13     anthu ake oponya mauta andizungulira.
Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga
    ndipo akutayira pansi ndulu yanga.
14 Akundivulaza kawirikawiri,
    akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo.

15 “Ndasokerera chiguduli pa thupi langa
    ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.
16 Maso anga afiira ndi kulira,
    ndipo zikope zanga zatupa;
17 komatu manja anga sanachite zachiwawa
    ndipo pemphero langa ndi lolungama.

18 “Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga;
    kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke!
19 Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba;
    wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.
20 Wondipembedzera ndi bwenzi langa,
    pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu;
21 iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu
    monga munthu amadandaulira bwenzi lake.

22 “Pakuti sipapita zaka zambiri
    ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.”