Add parallel Print Page Options

Lamba Womanga Mʼchiwuno

13 Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.” Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.

Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti, “Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.” Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.

Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.” Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.

Pamenepo Yehova anandiwuza kuti, “Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 10 Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu. 11 Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.

Zikopa Zothiramo Vinyo

12 “Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’ 13 Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu. 14 Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”

Yuda Adzapita ku Ukapolo

15 Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu,
    musadzitukumule,
    pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.
16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu
    asanagwetse mdima,
mapazi anu asanayambe kupunthwa
    mʼchisisira chamʼmapiri.
Asanasandutse kuwala
    mukuyembekezerako kukhala
    mdima wandiweyani.
17 Koma ngati simumvera,
    ndidzalira kwambiri
    chifukwa cha kunyada kwanu.
Mʼmaso mwanga
    mwadzaza ndi misozi yowawa
    chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.

18 Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti,
    “Tsikani pa mipando yaufumuyo,
pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo
    zagwa pansi.”
19 Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa
    ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula.
Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo,
    watengedwa yense ukapolo.

20 Tukula maso ako kuti uwone
    amene akubwera kuchokera kumpoto.
Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti,
    nkhosa zanu zokongola zija?
21 Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira
    anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira?
Kodi sudzamva zowawa
    ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
22 Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,
    “Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?”
Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri
    kuti zovala zanu zingʼambike
    ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
23 Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,
    kapena kambuku kusintha mawanga ake?
Inunso amene munazolowera kuchita
    zoyipa simungathe kusintha.

24 “Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu
    amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.
25 Limeneli ndiye gawo lanu,
    chilango chimene ndakukonzerani
chifukwa chondiyiwala Ine
    ndi kutumikira milungu yabodza,
            akutero Yehova.
26 Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso
    kuti umaliseche wanu uwonekere.
27 Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu
    ndi ziwerewere zanu,
zochitika pa mapiri ndi mʼminda.
    Tsoka iwe Yerusalemu!
Udzakhala wosayeretsedwa
    pa zachipembedzo mpaka liti?”