Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
One verse. Every morning. Get the free Verse of the Day email.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
Finding your way around? Take the tour.
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

Yeremiya 37  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atsekera Yeremiya Mʼndende

37 Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, inakhazika pa mpando waufumu Zedekiya mwana wa Yosiya kukhala mfumu ya Yuda. Iye analowa mʼmalo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu. 2 Koma Zedekiya kapena atumiki ake ngakhalenso anthu a mʼdzikomo sanasamalire mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya.

3 Tsono Zedekiya anatuma Yehukali mwana wa Selemiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga uwu: “Chonde tipempherereni kwa Yehova Mulungu wathu.”

4 Nthawi imeneyinso nʼkuti Yeremiya ali ndi ufulu woyenda pakati pa anthu chifukwa anali asanaponyedwe mʼndende. 5 Nthawi imeneyinso nʼkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka mʼdziko la Igupto. Ndipo Ababuloni amene anali atazinga Yerusalemu atamva zimenezi, anachoka ku Yerusalemuko.

6 Tsono Yehova anawuza mneneri Yeremiya kuti, 7 “Uyiwuze mfumu ya Yuda imene inakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa ine kuti Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, gulu lankhondo la Farao limene linatuluka kuti lidzakuthandize lidzabwerera kwawo ku Igupto. 8 Ndipo Ababuloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Iwo adzawugonjetsa ndi kuwutentha.

9 “Yehova akuti: Musadzinyenge, nʼkumaganiza kuti, ‘Ndithu Ababuloni adzatisiya.’ Ndithudi sadzakusiyani! 10 Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.”

11 Gulu lankhondo la Ababuloni litaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao, 12 Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu ndi kumapita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake. 13 Koma atafika pa Chipata cha Benjamini, mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, anagwira mneneri Yeremiyayo ndipo anati, “Iwe ukuthawira kwa Ababuloni!”

14 Yeremiya anati, “Zimenezo si zoona! Ine sindikuthawira kwa Ababuloni.” Koma Iriya sanamumvere. Mʼmalo mwake anagwira Yeremiya nʼkupita naye kwa akuluakulu. 15 Akuluakuluwo anamupsera mtima Yeremiya ndipo anamukwapula ndi kumuyika mʼnyumba ya mlembi Yonatani, imene anayisandutsa ndende.

16 Yeremiya anayikidwa mʼndende ya pansi pa nthaka, kumene anakhalako nthawi yayitali. 17 Kenaka Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akayitane Yeremiya ndipo anabwera naye ku nyumba ya mfumu. Atafika mfumu inamufunsa mwamseri kuti, “Kodi pali mawu ena amene Yehova wakuwuza?”

Yeremiya anayankha kuti, “Inde. Inu mfumu mudzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni.”

18 Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo kapena akuluakulu anu kapenanso anthu awa, kuti mundiyike mʼndende? 19 Kodi ali kuti aneneri anu amene anakuloserani kuti, ‘Mfumu ya ku Babuloni sidzakuthirani nkhondo pamodzi ndi dziko lino’? 20 Koma tsopano, mbuye wanga mfumu, chonde tamverani. Loleni ndinene pempho langa pamaso panu: Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuopa kuti ndingakafere kumeneko.”

21 Tsono Mfumu Zedekiya analamula kuti Yeremiya asungidwe mʼbwalo la alonda. Ankamupatsa buledi tsiku ndi tsiku amene ankamugula kwa ophika buledi. Anapitiriza kutero mpaka buledi yense anatha mu mzindamo. Choncho Yeremiya anapitirira kukhala mʼbwalo la alonda.

Next
Yeremiya 36
Yeremiya 38
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway