Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
Finding your way around? See how the new Bible Gateway works. Take the tour.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
One verse. Every morning. Sign up.
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

Mika 1  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.

2 Tamverani, inu anthu a mitundu yonse,
    mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo,
pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani,
    Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.

Chiweruzo cha Samariya ndi Yerusalemu

3 Taonani! Yehova akubwera kuchokera ku malo ake;
    Iye akutsika ndipo akuponda pa malo okwera a dziko lapansi.
4 Mapiri akusungunuka pansi pake,
    ndipo zigwa zikugawikana
ngati phula pa moto,
    ngati madzi ochokera mʼphiri.
5 Zonsezi ndi chifukwa cha cholakwa cha Yakobo,
    chifukwa cha machimo a nyumba ya Israeli.
Kodi cholakwa cha Yakobo nʼchiyani?
    Kodi si Samariya?
Kodi malo achipembedzo a Yuda ndi ati?
    Kodi si Yerusalemu?

6 “Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja,
    malo odzalamo mphesa.
Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa
    ndipo ndidzafukula maziko ake.
7 Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya;
    mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto;
    ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake.
Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere,
    mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.”

Kulira ndi Kumva Chisoni

8 Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni;
    ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche.
Ndidzafuwula ngati nkhandwe
    ndi kulira ngati kadzidzi.
9 Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika;
    chafika ku Yuda.
Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga,
    mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo.
10 Musanene zimenezi ku Gati;
    musalire nʼkomwe.
Mugubuduzike mu fumbi
    ku Beti-Leafura.
11 Inu anthu okhala ku Safiro,
    muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi.
Iwo amene akukhala ku Zanaani
    sadzatuluka.
Beti-Ezeli akulira mwachisoni;
    chitetezo chake chakuchokerani.
12 Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu,
    akuyembekezera thandizo,
chifukwa Yehova wabweretsa tsoka,
    lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.
13 Inu anthu okhala ku Lakisi
    mangani akavalo ku magaleta.
Inu amene munayamba kuchimwitsa
    mwana wamkazi wa Ziyoni,
pakuti zolakwa za Israeli
    zinapezeka pakati panu.
14 Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana
    ndi a ku Moreseti Gati.
Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama
    kwa mafumu a Israeli.
15 Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu
    okhala mu Maresa.
Ulemerero wa Israeli udzafika
    ku Adulamu.
16 Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira
    ana anu amene mumawakonda;
mudzichititse dazi ngati dembo,
    pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo.

Next
Yona 4
Mika 2
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway