Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
Finding your way around? See how the new Bible Gateway works. Take the tour.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
We’ve made some updates. Have feedback?
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

Mateyu 22  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Fanizo la Phwando la Ukwati

22 Yesu anayankhula nawonso mʼmafanizo, nati, 2 “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna. 3 Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.

4 “Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’

5 “Koma iwo sanalabadire ndipo anachoka; wina anapita ku munda wake ndi wina ku malonda ake. 6 Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha. 7 Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.

8 “Pamenepo anati kwa antchito ake, ‘Phwando laukwati lakonzedwa, koma amene ndinawayitana sanali oyenera. 9 Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’ 10 Pamenepo antchitowo anapita ku misewu nakasonkhanitsa anthu onse amene anakawapeza, abwino ndi oyipa omwe, ndipo nyumba ya madyerero inadzaza ndi oyitanidwa.

11 “Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati. 12 Inamufunsa kuti, ‘Bwenzi walowa bwanji muno wopanda zovala zaukwati?’ Munthuyo anakhala chete.

13 “Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’

14 “Popeza oyitanidwa ndi ambiri koma osankhidwa ndi ochepa.”

Za Kupereka Msonkho

15 Kenaka Afarisi anatuluka nakakonza njira zomupezera zifukwa Yesu mʼmawu ake. 16 Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani? 17 Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”

18 Koma Yesu podziwa maganizo awo oyipa anati, “Inu achiphamaso, bwanji mufuna kundipezera chifukwa? 19 Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari, 20 ndipo anawafunsa kuti, “Kodi chithunzi ichi ndi malemba awa ndi za ndani?”

21 Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.”

Pamenepo anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”

22 Atamva izi, anadabwa, ndipo anamusiya Iye, nachoka.

Ukwati ndi za Kuuka kwa Akufa

23 Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso. 24 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 25 Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo. 26 Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri. 27 Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso. 28 Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?”

29 Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu. 30 Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 31 Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti, 32 ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”

33 Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.

Lamulo Lalikulu Koposa

34 Pakumva kuti Yesu anawakhalitsa chete Asaduki, Afarisi anasonkhana pamodzi. 35 Mmodzi wa iwo, katswiri wa malamulo anamuyesa Iye ndi funso ndipo anati, 36 “Aphunzitsi, kodi lamulo lalikulu koposa mu malamulo ndi liti?” 37 Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse. 38 Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse. 39 Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ 40 Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”

Kodi Khristu ndi Mwana wa Ndani?

41 Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti, 42 “Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?”

Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.”

43 Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,

44 “Ambuye anati kwa Ambuye wanga:
    ‘Khala pa dzanja langa lamanja
mpaka ndiyike adani ako
    pansi pa mapazi ako.’

45 Ngati tsono Davide amamutchula ‘Ambuye,’ zingatheke bwanji kukhala mwana wake?” 46 Panalibe wina anatha kuyankha, ndipo kuchokera pamenepo, panalibe wina anayerekeza kumufunsa funso.

Next
Mateyu 21
Mateyu 23
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway