Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
Study Bibles + commentaries + Scripture = deeper understanding. Explore Bible Gateway Plus.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
Read Scripture without ads. Try Bible Gateway Plus.
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

Aroma 2  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kuweruza Kolungama kwa Mulungu

2 Choncho, iwe amene umaweruza munthu wina, ulibe pokanira pakuti nthawi iliyonse pamene uweruza wina ukudzitsutsa wekha chifukwa iwe amene umaweruzawe umachitanso zinthu zomwezo. 2 Tsopano ife tikudziwa kuti chiweruzo cha Mulungu, chotsutsa amene amachita zinthu zotere, nʼchokhazikika pa choonadi. 3 Kodi ukuganiza kuti udzathawa chiweruzo cha Mulungu iwe munthu wamba, pamene uweruza ena, iwe ndi kumachitanso zomwezo? 4 Kodi kapena ukupeputsa kukoma mtima kwa Mulungu, kuleza mtima kwake ndi kupirira kwake? Kodi sukuzindikira kuti kukoma mtima kwakeko, nʼkofuna kuti iweyo ulape machimo ako?

5 Koma pakuti ndiwe wosamvera ndi wa mtima wosafuna kulapa, ukudzisungira chilango pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu, pamene chiweruzo cholungama cha Mulungu chidzaonetsedwa. 6 Mulungu adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. 7 Iye adzapereka moyo wosatha kwa amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pochita ntchito zabwino mopirira. 8 Koma Mulungu adzakhuthulira mkwiyo ndi ukali wake pa amene amachita zofuna zawo ndi kukana choonadi nʼkumatsatira zoyipa. 9 Masautso ndi zowawa zidzagwera munthu aliyense amene amachita zonyansa, kuyambira Myuda kenaka anthu a mitundu ina. 10 Koma ulemerero, ulemu ndi mtendere zidzakhala kwa aliyense amene amachita zabwino, kuyambira Myuda kenaka anthu a mitundu ina. 11 Pajatu Mulungu alibe tsankho.

12 Onse amene amachimwa osadziwa Malamulo, adzawonongeka ngakhale kuti sadziwa Malamulowo. Ndipo onse amene amachimwa akudziwa Malamulo adzaweruzidwa potsata Malamulowo. 13 Pakuti si amene amangomva Malamulo amene amakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma ndi okhawo amene amachita zili mʼMalamulomo amene adzatchedwa olungama. 14 Ndithu, pamene a mitundu ina, amene alibe Malamulo, koma mwachikhalidwe chawo amachita zimene zili mʼMalamulo, iwowo ndi Malamulo pa iwo okha, ngakhale kuti alibe Malamulowo. 15 Ntchito zawo zimaonetsa kuti Malamulowo alembedwa mʼmitima mwawo. Chikumbumtima chawonso chimawachitira umboni pakuti maganizo awo amawatsutsa kapena kuwavomereza. 16 Izi zidzachitika pa tsiku limene Mulungu adzaweruza zinsinsi za anthu kudzera mwa Yesu Khristu, monga momwe Uthenga wanga Wabwino unenera.

Ayuda ndi Malamulo

17 Koma iweyo, amene umadzitcha kuti ndiwe Myuda, umadalira Malamulo, ndipo umanyadira ubale wako ndi Mulungu, 18 ngati umadziwa chifuniro chake, ndi kudziwa zoyenera kuchita chifukwa unaphunzitsidwa ndi Malamulo; 19 ngati umadziwadi kuti ndiwe mtsogoleri wa osaona, nyale yowunikira amene ali mu mdima, 20 mlangizi wa anthu opusa, mphunzitsi wa makanda, chifukwa umadziwa kuti mʼMalamulo uli nayo nzeru yonse ndi choonadi, 21 tsono, iwe amene umaphunzitsa ena, sudziphunzitsa wekha kodi? Kodi iwe amene umalalikira kuti anthu asabe, umabanso? 22 Kodi iwe amene umanena kuti anthu asachite chigololo, umachitanso chigololo? Kodi iwe amene umanyasidwa ndi mafano, umalandanso za mʼnyumba zopembedzera mafanowo? 23 Kodi iwe amene umadzitama ndi Malamulo, umamuchititsa manyazi Mulungu posamvera Malamulowo? 24 Monga kwalembedwa, “Dzina la Mulungu likuchitidwa chipongwe pakati pa a mitundu ina chifukwa cha inu.”

25 Mdulidwe umakhala ndi phindu ngati usunga Malamulo, koma ngati sumvera Malamulo, iweyo umakhala ngati kuti sunachite mdulidwe. 26 Ngati amene sanachite mdulidwe achita zomwe zili mʼMalamulo, kodi sadzatengedwa ngati ochita mdulidwe? 27 Munthu amene sanachite mdulidwe mʼthupi koma amamvera Malamulo adzakutsutsa iwe wosamvera Malamulowe, ngakhale kuti uli nawo Malamulo olembedwawo.

28 Myuda weniweni si amene angooneka ngati Myuda pamaso pa anthu, ndipo mdulidwe weniweni si umene umangochitika mʼthupi pamaso pa anthu. 29 Ayi, Myuda weniweni ndi amene ali Myuda mu mtima mwake, ndipo mdulidwe weniweni ndi wa mtima, wochitika ndi Mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ayi.

Next
Aroma 1
Aroma 3
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway