Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
Study Bibles + commentaries + Scripture = deeper understanding. Explore Bible Gateway Plus.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
Read Scripture without ads. Try Bible Gateway Plus.
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

Aroma 16  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mawu Olawirana

16 Ine ndikupereka kwa inu mlongo wathu Febe, mtumiki wa mpingo wa ku Kenkreya. 2 Ine ndikukupemphani kuti mumulandire mwa Ambuye mʼnjira yoyenera oyera mtima ndi kumupatsa thandizo lililonse limene akulifuna kuchokera kwa inu, pakuti iye wakhala thandizo lalikulu kwa anthu ambiri kuphatikiza ine.

3 Perekani moni kwa Prisila ndi Akura, atumiki anzanga mwa Khristu Yesu. 4 Iwo anapereka miyoyo yawo chifukwa cha ine. Osati ine ndekha komanso mipingo yonse ya a mitundu ina ikuyamika.

5 Perekaninso moni kwa mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo.

Perekani moni kwa mʼbale wanga wokondedwa Epeneto, amene ndi woyamba kukhulupirira Khristu mʼchigawo cha Asiya.

6 Perekani moni kwa Mariya, amene wakhala akukugwirirani ntchito kwambiri.

7 Perekani moni kwa Androniko ndi Yuniya abale anga amene anali mʼndende pamodzi ndi ine. Iwo amadziwika ndi atumwi, ndipo iwo anali mwa Khristu ine ndisanakhale.

8 Perekani moni kwa Ampliato, amene ine ndimamukonda mwa Ambuye.

9 Perekani moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu mwa Khristu ndi wokondedwa wanga Staku.

10 Perekani moni kwa Apele, woyesedwa ndi wovomerezeka mwa Khristu.

Perekani moni kwa a mʼbanja la Aristobulo.

11 Perekani moni kwa Herodiona, mʼbale wanga.

Perekani moni kwa a mʼbanja la Narkiso amene ali mwa Ambuye.

12 Perekani moni kwa Trufena ndi Trufosa, amayi aja amene amagwira ntchito ya Ambuye molimbika.

Perekani moni kwa mnzanga wokondedwa Persida, mayi winanso amene wagwira ntchito kwambiri mwa Ambuye.

13 Perekani moni kwa Rufo, wosankhidwa mwa Ambuye, ndi amayi ake, amene akhala amayi anganso.

14 Perekani moni kwa Asunkrito, Felego, Herima, Patroba, Herima ndi abale amene ali nawo pamodzi.

15 Perekani moni kwa Filologo, Yuliya, Neriya ndi mlongo wake, ndi Olumpa ndi oyera mtima onse amene ali nawo pamodzi.

16 Mupatsane moni wina ndi mnzake mwachikondi choona.

Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.

17 Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo. 18 Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa. 19 Aliyense anamva za kumvera kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.

20 Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu.

Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.

21 Timoteyo, mtumiki mnzanga, akupereka moni. Nawonso, Lusio, Yasoni ndi Sosipatro, abale anga akutero.

22 Ine Tertio, amene ndalemba kalatayi, ndi kupereka moni mwa Ambuye.

23 Gayo, amene chifukwa cha chisamaliro chake, ine ndi mpingo wonse kuno tikusangalala, akupereka moni.

Erasto, amene ndi msungichuma wa mzinda wonse ndiponso mʼbale wathu Kwato, akupereka moni.

24 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.

25 Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali, 26 koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye, 27 kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni.

Next
Aroma 15
1 Akorinto 1
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway