Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
Understand more as you read. Go deeper with Bible Gateway Plus.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
We’ve made some updates. Have feedback?
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

Ahebri 9  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kupembedza mʼTenti ya Dziko Lapansi

9 Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu. 2 Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika. 3 Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri. 4 Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano. 5 Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.

6 Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo. 7 Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira. 8 Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo. 9 Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo. 10 Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.

Magazi a Yesu

11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano. 12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. 13 Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi, 14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.

15 Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija.

16 Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi, 17 chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo. 18 Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi. 19 Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse. 20 Iye anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge.” 21 Momwemonso Mose anawaza magazi pa Chihema chija ndiponso pa zipangizo zonse zogwiritsa ntchito pa chipembedzo. 22 Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.

23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo. 24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife. 25 Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake. 26 Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. 27 Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa, 28 momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

Next
Ahebri 8
Ahebri 10
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway