Menu
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
account
Understand more as you read. Go deeper with Bible Gateway Plus.
Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo
Understand more as you read. Try Bible Gateway Plus.
  • Read
    • Reading Plans
    • Advanced Search
    • Available Versions
    • Audio Bibles
  • Study
    • Scripture Engagement
    • More Resources
  • News
  • Explore
    • Newsletters
    • Devotionals
    • Bible Gateway App
    • Bible Audio App
    • Take a Tour
  • Store
    • Bibles
    • Deals
    • More
  • Bible Gateway Plus
CCL
Version
Bible Books Bible Books
CCL
Version
Read
Study
News
Explore
Store
Bible Gateway Plus
Light Mode Dark Mode
Font Size
Log In show menu
Previous Next
Print PrintSettingsSettingsShare ShareParallelParallelExpandExpandCollapse

1 Akorinto 11  Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu.

Makhalidwe Oyenera pa Mapemphero

2 Ndikukuyamikani chifukwa chondikumbukira pa zonse ndiponso posunga ziphunzitso monga ndinakuphunzitsirani. 3 Tsopano ndikufuna muzindikire kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, ndipo mwamuna ndiye mutu wamkazi, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu. 4 Mwamuna aliyense wopemphera kapena kunenera ataphimba mutu wake akunyoza mutu wakewo. 5 Ndipo mkazi aliyense wopemphera kapena kunenera asanaphimbe mutu wake sakulemekeza mutu wakewo. Kuli chimodzimodzi kumeta mutu wake. 6 Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake.

7 Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna. 8 Pakuti mwamuna sachokera kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna. 9 Ndipo mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna. 10 Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake. 11 Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi. 12 Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu.

13 Dziweruzeni. Kodi nʼchabwino kuti mkazi apemphere kwa Mulungu wopanda chophimba kumutu? 14 Kodi chikhalidwe chathu sichitiphunzitsa kuti nʼchamanyazi kuti mwamuna akhale ndi tsitsi lalitali, 15 koma mkazi akakhala ndi tsitsi lalitali ndi ulemerero wake? Pakuti mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali monga chophimba kumutu. 16 Ngati wina akufuna kutsutsapo pa zimenezi, ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe machitidwe ena apadera koma ndi omwewa.

Mgonero wa Ambuye

17 Koma popereka malangizo awa sindikufuna kukuyamikirani popeza mʼmisonkhano yanu mumachita zoyipa kuposa zabwino. 18 Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona. 19 Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu. 20 Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye. 21 Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera. 22 Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni.

23 Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye ndi zomwe ndinakupatsani. Ambuye Yesu, usiku umene anaperekedwa uja, anatenga buledi. 24 Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.” 25 Chimodzimodzi, atatha kudya, anatenga chikho, nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga; imwani nthawi zonse pokumbukira Ine.” 26 Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.

27 Chifukwa chake, aliyense amene adya buledi kapena kumwa chikho cha Ambuye mʼnjira yosayenera adzachimwira thupi ndi magazi a Ambuye. 28 Munthu adzisanthule yekha asanadye buledi kapena kumwa chikhochi. 29 Popeza aliyense amene adya kapena kumwa mosazindikira thupi la Ambuye, amadya ndi kumwa chiweruzo chake chomwe. 30 Nʼchifukwa chake pakati panu ambiri mwa inu ndi ofowoka ndi odwala, ndipo ambirinso agona tulo. 31 Koma tikanadziyesa tokha sitikaweruzidwanso. 32 Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

33 Ndiye tsono abale anga, pamene musonkhana pa chakudya, mudikirirane. 34 Ngati wina ali ndi njala, adye ku nyumba kwake kuti pamene musonkhana pamodzi zisafike poti muweruzidwe nazo.

Ndipo ndikabwera ndidzakupatsani malangizo ena owonjezera.

Next
1 Akorinto 10
1 Akorinto 12
Next
dropdown
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Bible Gateway Plus logo
Bible Gateway logo

Font Size

Font Size

Dark Mode

Light Mode Dark Mode

About

  • About
  • Learn About the Bible
  • Statement of Faith
  • Mobile App
  • Store
  • Blog
  • Newsroom
  • Support Us

Help

  • FAQs
  • Tutorials
  • Use Bible Gateway on Your Site
  • Advertise with us
  • Contact us
  • Privacy policy
  • California Privacy Rights
  • Do Not Sell My Personal Information
  • Site: Terms of use
  • Widget: Terms of use

Our Network

  • FaithGateway
  • StudyGateway
  • ChurchSource
  • HarperCollins Christian Publishing
  • Grupo Nelson
  • Editorial Vida
  • Thomas Nelson
  • WestBow Press
  • Zondervan
  • MasterLectures

Social

  • Facebook
  • Instagram
  • Pinterest
  • TikTok
  • X
  • YouTube

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway
Sign Up for Bible Gateway: News & Knowledge
Get weekly Bible news, info, reflections, and deals in your inbox.

By submitting your email address, you understand that you will receive email communications from Bible Gateway, operated by HarperCollins Christian Publishing, 501 Nelson Pl, Nashville, TN 37214 USA, including commercial communications and messages from partners of Bible Gateway. You may unsubscribe from Bible Gateway’s emails at any time. If you have any questions, please review our Privacy Policy or email us at privacy@biblegateway.com.

Preferences

  • Versión en español
  • Preferences
  • Classic Bible Gateway